Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Aphunzitsi Achikatolika M’boma La Zomba Awayamikira Kamba Kothandiza Odwala

$
0
0

Aphunzitsi abungwe la chikatolika ku parish ya Mayaka  m’boma la Zomba awayamikira chifukwa cha chidwi chawo chofuna kuthandiza odwala.

Mmodzi mwa akulu akulu pa chipatala cha chikulu cha Zomba Mayi Emma Chikaya anena izi pomwe aphunzitsi akwa mayaka anakacheza ndikukapereka mphatso zawo pa chipatala cha Zomba.

“Kubwera kwa iwowaw kukupereka uthenga woti tiyenera kugawana kangachepe komwe tili nako ndipo zithandiza odwalawa kuzindikira kuti kunjaku kulinso anthu amene amawakumbukira,” anatero mayi Chikaya.

mmodzi mwa aphunzitsi achikatolika wa mayi Mary Ganiza anati achita izi malinga ndi pempho la a Papa mu chaka ichi cha chifundo cha Mulungu.

“Ifeyo ngati aphunzitsi tinawona kuti tikhale patsogolo kuphunzitsa anthu kuti tikhale achifundo monga a Papa athu akunenera,” anatero mayi Ganiza.

Katundu yemwe aphunzitsiwa apereka ndi monga sopo, sugar ndiponso ufa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875