Dziko la Germany lati litseka zina mwa zipata zake ndi dziko la Australia pofuna kuchepetsa anthu othawa kwawo omwe akulowa m`dzikolo kudzera mdziko la Australia lo.
Akuluakulu a dziko la Germany ati akudandaula kamba kosowa mgwirizano pakati pa mayiko awiriwa zomwe zikuchititsa kuti dziko la Germany lilephere kuthandiza mokwanira anthu omwe akulowa m`dzikolo.
Pakadali pano anthu othawa kwawo akulowanso m`dziko la Germany kudzera m`dziko la Greece ngakhale kuti kuli nyengo yozizira.
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC anthu makumi awiri omwe ambiri ndi ana afa boti lomwe anakwera litamira m`dziko la Greece pomwe amafuna kuwoloka paulendo wawo wa m`maiko akuulaya.
Dziko la Germany lati litseka zina mwa zipata zake ndi dziko la Australia pofuna kuchepetsa anthu othawa kwawo omwe akulowa m`dzikolo kudzera mdziko la Australia lo.
Akuluakulu a dziko la Germany ati akudandaula kamba kosowa mgwirizano pakati pa mayiko awiriwa zomwe zikuchititsa kuti dziko la Germany lilephere kuthandiza mokwanira anthu omwe akulowa m`dzikolo.
Pakadali pano anthu othawa kwawo akulowanso m`dziko la Germany kudzera m`dziko la Greece ngakhale kuti kuli nyengo yozizira.
Malinga ndi malipoti awailesi ya BBC anthu makumi awiri omwe ambiri ndi ana afa boti lomwe anakwera litamira m`dziko la Greece pomwe amafuna kuwoloka paulendo wawo wa m`maiko akuulaya.v