Akuluakulu a dziko la China ati amanga episkopi wodzalowa m’malo mwa bishop wopuma wa mpingo wakatolika ndi kumuchotsa ku dayosizi yomwe amatumikira pofuna kuti asakhazikitsidwe kukhala episkopi watsopano wa dayosiziyo.
Ambuye Peter Shao omwe amatumikira mu dayosizi ya Wenzhou awagwira, yemwe anali episkopi wa dayosiziyo Ambuye Vincent Zhu atamwalira ndi matenda a khansa.
Malipoti a Catholic Culture ati ambuyewa akusungidwa mchigawo cha kumpoto cha kuzambwe kwa dziko la China komwe ndi mtunda wautali ndi dayosiziyo.
Malinga ndi malipoti Ambuye Shao anachotsedwa pa nthawiyo ndi cholinga choti asakhale nawo pa mwambo wa maliro wa Ambuye Zhu.
Ambuye Shao ati siwololedwa kukhala episkopi kaamba koti siwovomerezedwa ndi boma la dziko la China.