Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

MANEB Yakweza Malipiro a Mayeso

$
0
0

Bungwe lowona za mayeso m’dziko muno la Malawi National Examinations Board (MANEB) lakweza ndalama zomwe ophunzira a standade 8 komanso a form 4 akuyenera kulipilira ku bungweli kuti alembe mayeso.

Mneneri wa bungweli a Simeon Maganga ati padakali pano ophunzira a standade 8akuyenera kulipira 1500kwachaya chitupa cholembera mayeso  ndipo a form 4 akuyenera kulipira 800 kwacha pa phunziro lililonse kuchoka pa 400 kwacha ndipo akuyeneranso kulipira 2000 kwacha ya chitupa cholembera mayeso.

“M’chaka cha 2014 tinapempha ku boma kuti tikweze malipiro kuchoka pa 84 kwacha poyamba paja kufika pa 800 kwacha. Anatilora koma anatiuza kuti tikweze ndi theka kenako tizamalizenso ndi theka linalo. Choncho chaka chatha ophunzira amalipira 400 kwacha pa phunziro lililonse. Tsopano chaka chino tikumalizitsa theka linalo m’chifukwa chake a form 4 azilipira 800 kwacha pa phunziro lililonse ndipo chitupa cholembera mayeso azilipira 2000 kwacha. Kwa a standade 8 mayeso ndi a ulere koma chitupa cholembera mayeso ndi 1500 kwacha,” anatero a Maganga.

Iwo ati bungwe la MANEB lachita izi pofuna kuwonetsetsa kuti likupititsa patsogolo maphunziro m’dziko muno popereka mayeso apamwamba kwa ophunzira.

“Tachita izi kuti mayeso athu apitirire kukhala apamwamba chifukwa ngati tilibe ndalama ndiye kuti sizitichitira ubwino. Tikufuna tichepetse chinyengo kuti ana olemba mayeso akhale enieni osati zolemberana mayeso. Sitikufuna olemera azidyera masuku pa mutu anthu amene ali osauka. Zomwe tikuchitazi tikuti tithandize ovutika. Tikafuna zinthu zotsika mtengo nthawi zambiri zimakhala kuti si zapamwamba,”anatero a Maganga.

Iwo ati anthu asawone kuchuluka kwa ndalama zomwe azilipira ku bungweli koma awone kufunika kwa mapepala omwe ophunzirawa apeze kaamba koti ati mayeso amalembedwa kamodzi kokha koma pamene masatifiketi amakhala nawo mpaka kalekale.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>