Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse papa Francisco wapempha atolankhani kuti asagwiritse ntchito yawo kukhala chida chowonongera zinthu.
Papa Francisco wanena izi ku Vaticanpa mkumano omwe anali nawondikhonsolo ya m’dziko la Italy yoona za atolankhani.
Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu anati atolankhani akuyenera kulemekeza chikhalidwe cha munthu aliyense ndipo kuti asamagwiritse ntchito yawo ngati chida choonongera kapena kuwopsezera anthu.
Papa wati kudzudzula pa zoipa ndikovomerezeka koma wati kukuyenera kuchitika mwaulemu zomwe ati zingapititse dziko patsogolo.
Papa Francisco wati atolankhani ndi ofunikira kwambiri ndipo ali ndi udindo waukulu pa ntchito zotukukula miyoyo ya anthu.