Bungwe la za umoyo lomwe si la boma la Blantyre Institute for Community Ophthalmology (BICO) lapeleka thandizo la ndalama zokwanira 5 Hundred Thousand Kwacha ku chipatala cha boma la Mangochi.
Polankhula pa mwambo wopeleka thandizolo m’modzi mwa akulu-akulu m’bungwe-li a Ignasio Kachepa anati bungweli lapeleka thandizoli ndi cholinga chofuna kuchepetsa mavuto osiyanasiyana amene chipatalachi chikukomana nawo.
Iwo anati ndalamazi anapereka ndi cholinga choti chipatalachi chigulire chakudya cha odwala pa chipatalachi.
“A BICO takhala tikugwira ntchito m’boma la Mangochi kwa ka nthawi ndiye tinawona kuti tithandizepo mavuto ena amene ali pa chipatala pano.Tinawafunsa akuluakulu apa chipatalachi ndipo anatiuza kuti titathandiza mbali ya zakudya zingakhale bwino, ndi chifukwa chake tabwera ndithandizo la ndalamazi kuti agulire chakudya cha odwala,”anatero a Kachepa.
Polankhulapo wogwilizira mkulu wa chipatala cha Mangochi aJames Kumwendaanathokoza bungweli kamba kothandiza chipatalachi zomwe anati zichepetsa mavuto a chakudya omwe chipatalachi chikukumana nawo padakali pano.
“Tikuthokoza a BICO kamba ka thandizo lawo lomwe labwera mu nthawi yake yomwe chipatala chathu chikukumana ndi vuto lakusowa kwa chakudya. Ndalamayi tigulira chakudya cha odwala pa chipatala pano omwe padakali pano akudya kawiri patsiku koma ndi thandizoli ndiye kuti ayamba kudya katatu pa tsiku,” anatero a Kumwenda.
Iwo apempha mabungwe ena omwe si aboma komanso anthu ena akufuna kwabwino kuti athandize chipatalachi ndi chakudya kamba koti ati chipatalachi chikukumana ndi mavuto aakulu akusowa kwa chakudya cha odwala.