Anthu otsatira chipani chotsutsa boma cha Malawi Congress(MCP)okhala m’dera la kum’poto cha kumadzulo m’boma la Salima apempha mtsogoleri wa chipanichi Dr. Lazarus Chakwera kuti athetse kusamvana komwe kwakula m’chipanichi.
Wapampando wa anthu okhudzidwa m’derali yemwenso ndi mkhalakale pa ndale m’dziko muno a Peter Nkosi wanena izi potsatira kuyimitsidwa kwa phungu wa derali Dr. Jessie Kabwira m’chipanichi.
A Nkosi ati kukambirana ndi njira yokhayo imene ingathetse mavuto omwe akula m’chipanichi.
“Mankhwala athu mu chipani chathu cha MCP ndi kukambirana. Ngati pali vuto tikuyenera tikambirane ndi kuthetsa vutolo. A Chakwera amayenera kumuitana Jessie ndikukambirana naye ndikuthetsa kusamvana kwawo. Ngati zikuvuta akanatiuza eni akefe timulange tokha chifukwa tinamusankha ndife,” anatero a Nkosi.
A Nkosi ati mpungwepungwe womwe ukuchitika m’chipanichi uchititsa zipani zina kupezerapo mwayi ndi kuzapambana pa chisankho cha 2019 komanso anati zisokoneza zitukuko zosiyanasiyana zomwe phungu wa derali Jessie Kabwira akuyenera kupereka ku derali.
“Anthu akuti Jessie amuchotsa m’chipani chifukwa sakugwirizana ndi a Chakwera komanso ati ife anthu a kuno ku Salima Northwest Constituency sitikugwirizana naye zimene sizili zowona. Zomwe zikuchitikazi zipereka mpata kwa zipani zina kuti zizachite bwino pa chisankho komanso zisokoneza zitukuko zomwe phungu wathuyu wakhala akuchita ku dera kuno. Ife phungu wathu kuno ndi Jessie Kabwira basi,” anatero aNkosi.
A Nkosi ati ngati phungu wa derali Jessie Kabwira sabwezeretsedwa mu chipanichi salola kuti kuderali kupezekenso chipani cha MCP.