Abwenzi a Radio Maria Malawi ochokera ku parishi ya Nguludi mu arkidayosizi ya Blantyre alonjeza kuti apitiriza kuthandiza wailesiyi mu zosowa zake ndi cholinga choti ipitirize kufalitsa uthenga wa Mulungu.
Wapampando wa abwenzi a Radio Maria Malawi m’parishiyi a Mike Duwa ndi omwe alankhula izi atayendera nthambi ya wailesiyi ya Limbe komwe mwazina amakamva mavuto omwe wailesiyi ikukumana nawo.
A Duwa ati abwenzi a wailesiyi ku parishi yawo apitiriza kuthandiza wailesiyi maka pa nthawi ino imene ikukumana ndi mavuto osiyanasiyana.
Polankhulapo m’modzi mwa otumikira ku nthambi ya Limbe ya wailesiyi a PaulSamudeni anathokoza abwenzi wa kaamba koyendera nthambi ya wailesiyi ndi kumva mavuto omwe nthambiyi ikukumana nawo.