Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Alimi Aleke Kudalira Mbewu ya Fodya

$
0
0

Pamene malonda afodya akupitilira kuvuta pa msika wa Auction, alimi mdziko muno awapempha kuti asiye kudalira mbewu ya fodya ndipo m’malo mwake apeze mbewu zina m’malo mwa mbewuyi.

M’modzi mwa akatswiri pa nkhani za ulimi mdziko muno yemwenso ndi phungu wa kunyumba ya malamulo wa dera la pakati m'boma la Salima a Felix Jumbe wanena izi pambuyo pa ulendo wake  wa m’maiko a Kenya ndi America komwe amakachita mkumano wa akatswiri a zaulimi mu Africa.

A Jumbe ati anthu akuyenera kuleka kutsata njira za makolo ndipo atsate njira zamakono pa ulimi wawo ndi kutenga ulimi ngati bizinesi.

Iwo anati, “Tikhonza kusintha; kusiya kudalira fodya mkutenga mbewu ya mtedza kukhala mbewu ya mlowam’malo wa fodya.

Iwo ati pa ulendo wawo wa m’dziko la Kenya komanso kudzera mu mkumano womwe anali nawo mdziko la America aphunzira zambiri zomwe zingathandize potukula ntchito za ulimi mdziko muno.

“Ku Kenya tinakumana akatswiri a za ulimi m’maiko amu Africa kudzera mu bungwe la Africa Green Revolution limene likuthandiza mayiko osiyanasiyana kuti atukuke komanso ulimi upite patsogolo. Umakhala msonkhano wa pa chaka maiko kuphunzira kuchokera ku dziko lina kuti tipindule. Timakakambirana kuti ulimi wathu m’Malawi muno usinthe ukhale wonga wa m’maiko ena woti anthu amapanga nawo ndalama zomwe zikuthandizira kuti maiko atukuke,” anatero a Jumbe.

Iwo ati ku mkumano wawo apezanso kuti ngongole kwa alimi zikuvuta zomwe zikuchititsa kuti alimi ambiri asamapindule ndi ulimi wawo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>