Anthu okwiya awononga katundu pa kampani yolima tea ya Mphezu kwa Bvumbwe m’boma la Thyolo potsatira imfa ya munthu wina yemwe wafa atamenyedwa ndi alonda a pa malowa.
Malinga ndi mtolankhani wathu amene anathamangira ku malowo pa nthawi ya chipolowechi anthuwa omwe ndi ochokera m’midzi ya Namaona, Foliji komanso Samuti awononga katundu osiyanasiyana pa kampani yi ati pokwiya ndi imfayi.