Wansembe wina wa mpingo wa katolika m’dziko la Mexicoyemwe anasowa atatengedwa ndi zigawenga wapezeka atafa pa malo ena mdzikolo.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, thupi la wansembeyi Jose Alfred Lopez lapezeka loweruka pafupi ndi m’zinda wina m’dzikolo.
Akuluakulu a tchalitchi lomwe wansembeyuamatumikira ati bambowa anatengedwa kunyumba kwawo ndi zigawenga zosadziwika lolemba sabata yatha ndipo tsiku lomwe bamboLopezanasowalo matupi a ansembe ena awiri omwenso anasowa mdzikolo anapezeka m’mbali mwa msewu wina atafa.
Malinga ndi malipoti chiwerengero cha ansembe omwe akhala akuphedwa mdziko la Mexico kuyambira m’chaka cha 2012 kufikira chaka chino ati tsopano chafika pa 15.