Bungwe lomenyera ufulu wa anthu mdziko muno la Human Rights Defender lapempha boma kuti lichite kafukufuku okwanira okhuzana ndi kupsa kwa misika m’dziko muno.
Mkulu wa bungweli a Billy Mayaya ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawipotsatira kupsa kwa msika wa mu mzinda wa Lilongwe.
Iwo ati akudabwa kuti mpaka pano boma silikupereka yankho pa zakupsa kwa misika m’dziko muno zomwe ati zikupereka chiopsezo kwa anthu omwe amadalira malonda.