Anthu ena ozungulira dera la mfumu Chikho mboma la Ntchisi avulaza abale a mfumu ya deralo komanso kuwononga katundu wa ndalama zoposa 117 thousand pokwiya ndi ulamuliro wa mfumuyo.
Mneneli wa apolisi mbomalo seagent Gladson M’bumpha watsimikiza za nkhaniyi. A M’bumpha ati anthuwo anatsogoleredwa ndi a Ziyendammanja Chunga, Kapalamula Nkhoza komanso a Kankhulukute Mapulanga.
“Chomwe tingapemphe mtundu wa a Malawi ndichoti ngati pali vuto pa nkhani za ufumu ndi bwino kupita kwa bwanankubwa wa bomalo osati kupanga zipolowe”, atero a M’bumpha.
Pakadali pano apolisi akuti ali mkati mofufuza kuti agwire anthu omwe akukhudzidwa kuti akayakhe milandu yowononga katundu komanso kuvulaza anthuwo.