Amuna awiri afa atakhudzidwa ndi ngozi zapansewu ziwiri zosiyana zomwe zachitika dzulo m’boma la Mangochi. Wachiwiri kwa w
Amuna awiri afa atakhudzidwa ndi ngozi zapansewu ziwiri zosiyana zomwe zachitika dzulo m’boma la Mangochi.
Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Amina Tepani Daudiwatsimikiza za ngozi ziwirizi ndipo wati amunawa ndi a Elias Lubwede a zaka 25 komanso a Felix Phiri a zaka 38 zakubadwa.
Sergeant Daudi wati a Lubwede anagundidwa ndi galimoto limene linali pa liwiro la mphamvu pamene amayenda mbali mwa nsewuwu pamene galimoto la a Phiri linagubuduzika kamodzi litaphulika teyala.
Pa ngozi ziwirizi anthu enanso avulala kwambiri ndipo agonekedwa pa chipatala cha boma la Mangochi.
Padakali pano apolisi m’bomali apempha onse oyendetsa galimoto kuti azikhala osamala komanso azichepetsa liwiro pamene akuyendetsa galimoto kuti apewe ngozi za pa nsewu.