Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Chigawenga cha IS Chaphedwa

$
0
0

Munthu wina yemwe akumuganizira kuti ndi wa gulu la zigawenga za Islamic State IS akuti amupha pomuombera mdziko la Turkey.

Malinga ndi malipotia wailesi ya BBC, mkuluyu wagwidwa mu mzinda wa Ankara, usiku wapitawu ndi asilikali adzikolo ali ndi mabomba omwe akuganiza kuti amafuna kuphulitsira mzindawu.

Malinga ndi malipoti, asilikali adzikolo anamutengera mkuluyu ku chipinda china cha m’mwamba kwambiri mu mzinda womwewo komwe anamupha pomuombera.

Panthawiyi anthu a mu mzindawu amachita mwambo wokonzekera chisangalalo choti Turkish Republic yakwanitsa zaka 29 chiyikhanzikitsireni, chomwe chichitike pa 10 mwezi wa mawa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>