Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wapempha Anthu Athandize Osowa Chakudya, Malo Abwino

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse PapaFransisco wapempha anthu akufuna kwabwino kuti azithandiza anthu amene akusowa chakudya komanso malo okhala abwino.

Papa wanena izi pa bwalo la St. Peters Square ku likulu la mpingowu ku Vatican pa mwambo womwe umachitika lachitatu liri lonse pomwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu amalankhula ndi anthu omwe anasonkhana pa bwaloli.

Mwa zina, Papa wapempha anthu kuti azikhudzidwa ndi kuvutika kwa ena ndipo azichitapo kanthu monga ankachitira Yesu Khristu komanso anthu ena omwe mpingo wa katolika umawatchula kuti ndi oyera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875