Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Akhale Odzidalira-DMI

$
0
0

Anthu mdziko muno awapempha kuti azikhala olimbikira ndi odzidalira pofuna kupititsa patsogolo chitukuko cha m’madera omwe akukhala.

M’modzi mwa akuluakulu oyendetsa ntchito zaDMIWomen’s Worldm’boma la Mangochi a Sampson Zalimba anena izi pa maphunziro a tsiku limodzi omwe bungweli linakonzera ena mwa amayi omwe akupezeka m’bomali.

Iwo ati amakondwera akamaona anthu makamaka amayi akugwira ntchito modzidalira posayembekera thandizo la ena.

“Amayi akhale ozidalira pawokha osamango dalira amuna kuti awachitire zinthu chifukwa nawonso ali ndi kuthekera,” anatero a Zalimba.

Bungweli limalimbikitsanso amayi omwe anapezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi kuti azimwa mankhwala motsatira ndondomeko komanso kuwapatsa uphungu wokhudza umoyo wawo.

Mwa zina amayiwa adandaula kuti akusalidwa ndi mafumu a m’madera mwawo mu zitukuko zosiyanasiyana.

“Samatiwerengera nkhani za makoponi, fetereza ndi zina ati kamba koti ndife ofa kale. Koma chiyambireni 2010 mpaka lero palibe wafa ngakhale mmodzi,” anatero mmodzi mwa amayiwa.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>