Anthu a m’dera la Mfumu Yaikulu Amidu m’boma la Balaka awapempha kuti akalembetse mwaunyinji mu kaundula wa chisankho kuti akhale ndi mwayi wodzaponya voti pa chisankho cha chaka cha mawa.
Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana m’bomali, la National Initiative For Civic Education (NICE), a Nelson Nkhoma alankhula izi pa sukulu ya Nangulukutiche pa msonkhano wophunzitsa anthu za chisankho.
Iwo ati, kuti anthu adzasankhe atsogoleri a ku mtima kwawo akuyenera kukhala ndi chitupa chovotera chimene angachipeze pokalembetsa mukaundula.
“tikufuna tidziwitse anthu akumidzi za chisakho chapatatu kamba koti aka ndi koyamba kukhala nacho kuno ku Malawi. Anthu tikuwaphunzitsa ntchito za makhasala , aphungu aku nyumba ya malamulo komanso pulezidenti”,atero a Nkhoma.
Mkuluyu wati bungwe lawo likuyesetsa kufikira madera akumidzi kuti afalitse uthenga wa chisankhowu kwa anthu amene amalephera kuulandira.
Kalembera wa voti m’boma la Balaka adzachitika magawo awiri. Gawo loyamba lizakhala kuyambira pa 11 mpaka 24 September m’madera apakati chakummawa, dera la kummwera ndi kuzambwe kwa bomali. Ndipo gawo lachiwiri la kalemberayu lidzachitika kuyambira pa 28 September mpaka pa 11 October ku dera lakumpoto kwa boma la Balaka.