Apolisi asanu ndi m’modzi 6 komanso anthu ena 16 afa pa chiwembu chomwe gulu la za uchifwamba la Islamic state lachita pa nyumba za boma mu mzinda wa Kirkuk mdziko la Iraq.
Malipoti a wailesi ya BBC ati asilikali a gulu la Islamic state okwana khumi ndi awiri 12 aphedwanso.
Malipoti ati izi zikuchitika pamenenso kumenyana kwa asilkali a dzikolo ndi zigawengazi mdera la Mosul kukupitilira pamene asilikali a dzikolo akufuna kulanda deralo m’manja mwa zigawengazi.
Mapemphero a tsiku la lero lachisanu alephereka mdzikolo kaamba koti mizikiti yonse ndi yotseka kaamba koopa kuchitidwa chiwembu ndi zigawengazi.