Bungwe la aphunzitsi losunga ndi kubwereketsa ndalama la SACCO m’chigawo cha pakati lapereka zipangizo zogwiritsa ntchito pa chipatala cha boma la Dedza.
Malinga ndi wamkulu wa bungweli a Henry Chowawa katundu amene waperekedwayi ndi monga makina othandizira munthu kupuma, makina ochotsera magazi kapena malovu mkamwa kwa munthu wovulala pa ngozi ndipo ndi za ndalama zokwana 2 million kwacha.
Iwo ati anaganiza zopereka katunduyi ku chipatala cha Dedza kaamba koti chipatalachi chimathandiza anthu a mzigawo zonse za dziko lino maka amene adwala kapena kuchita ngozi mu nsewu wopita ku Lilongwe.
“Tsikuli timakumbukira ma SACCO onse padziko lonse lapansi komanso kuchita ntchito zothandiza pa chitukukop cha dziko lino. Chipatala cha Dedza chimathandiza anthu a dziko lonse la Malawi chifukwa chili m’mbali mwa nsewu waukulu wa M1. Katundu amene taperekayu wambiri ndi okhudza kuthandizira anthu amene avulala pa ngozi chifukwa anthu ambiri akachita ngozi mu nsewu wa M1amathamangira nawo pa chipatalachi,” anatero a Chowawa.
Polankhulapo m’malo mwa bwanamkubwa wa bomali mayi Mwimbaanayamikira bungwe la SACCO mchigawochi kaamba ka thandizoli zomwe ati zichepetsa ena mwa mavuto omwe anali pa chipatalachi.
“Mukuchita bwino ndipo tikupempheni mupitirize. Boma liri pambuyo panu tikuthandizani. Padakali pano tikukonza ndiondomeko za momwe tingathandizire ma sacco ndi ma cooperative,” anatero mayi Mwimba.