Mabungwe omwe siaboma amene akugwira ntchito zao m’boma la Balaka, awapempha kuti azigwira ntchito zawo mopanda chinyengo komanso mofuna kutukula miyoyo ya anthu mbomalo.
Wapampando watsopano wa komiti ya mgwirizano wa mabungwe a m’bomali, ya Balaka Civil Society Organisations Network a Simplex Chithyola ndi omwe alankhula zimenezi atangosankhidwa kumene pa mpandowu. A Chithyola ati komitiyi iwonetsetsa kuti mabungwe onse omwe siaboma akutumikira anthu m’bomali moyenerera.
“Tiwonetsetsa kuti mabugwe omwe si aboma akugwira ntchito zomwe anabwerera kuno ku Balaka. Izi zithandiza kuti mabugwewa azigwira ntchito molongosoka zomwe zipindulitse anthu ambiri”, atero A Chithyola.