A kulikulu la mpingo wakatolika m’dziko muno ku Episcopal Comference of Malawi(ECM) alengeza za imfa ya bambo Cosmass Maleka omwe amatumikira mpingo-wu mu dayosizi ya Dedza.
Bambo-wa amwalira galimoto la mtundu wa Mini-Bus litawomba njinga ya moto yomwe bambo-wa anakwera. Ngoziyi yachitikira mu msewu wina m’dera la Dzoole m’boma la Ntcheu.
Malemu bambo Maleka anadzodzedwa unsembe m’chaka cha 2008. Iwowa anali ochokera ku parish ya Chipoka, koma amwalira akutumikira ku parish ya Mzama mu dayosizi-yo.
Thupi la malemu bambo Cosmass Maleka aliyika m’manda lachinayi pa 3 November ku manda a ansembe ku Bembeke Cathedral mu dayosizi ya Dedza.
Mzimu wa bambo Cosmas Maleka uwuse mu mtendere wosatha.