Akhristu a m’parishi ya Holy Family Cobbe Barracks mu dayosizi ya Zomba awayamikira kaamba kodzipereka pomanga tchalitchi latsopano lalikulu komanso lokongola.
Episkopi wopuma wa dayosiziyi Ambuye Allan Chamgwera ayamikira akhristuwa pamene anakayendera tchalitchili.
Ambuye Chamgwera apempha akhristu a mu parishiyi kuti tchalitchili likhale nyumba yozamitsa chikhristu kuti anthu ambiri apeze chipulumutso.
“Ndine wokondwa kwambiri kuti tchalitchili lomwe linayamba ine ndili bishop tsopano latha ndipo ndi lokongola chotere. pamene nyumbayi yamangidwa ikhale nyumba yolemekezeka ankhristu ayigwiritse ntchito moyenera kuti apezeremo chipulumutso. tchalitchili lamangidwa chonchi kamba ka kudzipereka kwa akhristu a parishi ino,” anatero Ambuye Chamgwera.
Polankhulapo Catechist wa parishiyi a Ronald Mukhura anathokoza ambuye opumawa kaamba koyendera akhristu a mparishiyi ndi kudzawalimbikitsa.
“Tinawaitana ambuye wa kuti adzakhale nafe chifukwa ndi amene anadzala mwala wa maziko wa tchalitchi limeneli nthawi imeneyo ali episkopi wa dayosizi ino. Iwowa ndi tate wathu, gogo wathu komwe timakapempha malangizo pena ndi pena zikasokonekera. Akhristu akuyenera kutengapo gawo powathandiza mu njira zosiyanasiyana chifukwa akusowa chisamaliro chathu,” anatero Catechist Mukhura.
Pa tsikuli, akhristu a mparishiyi anaperekanso zovala komanso sopo ndi katundu wina kwa akayidi a ndende ya Zomba ngati mbali imodzi ya Chaka cha chifundo cha mulungu.
Ambuye Chamgwera anati ndi okonzeka kupita kuparishi iliyonse mu dayosiziyi kukayendera akhristu awo pokhapokha ngati ali bwino komanso akhristuwo atsata dongosolo loyenera.