Mtsogoleri wa chipani cha National Salvation Front NASAF a JAMES NYONDO watsindika kuti ntchito yomwe walonjeza yopeleka ngongole ya ma TRACTOR kwa alimi a m’dziko muno siyankhambakamwa chabe ndipo ayikwanilitsa.
A Nyondo anena pomwe amafotokozera mtolankhani wathu zambiri za ntchitoyi komanso kuonetsa alenso omwe agwire nawo ntchitoyi ochokera m’dziko la AMERICA. Iwo ati anthu omwe apeze mwayi wa ngongolezi asadele nkhawa kamba koti ndi zosavuta kubweza.