Unduna woona zachilengedwe ndi kusintha kwa nyengo wati ugwira ntchito ndi unduna wa zamaphunziro ndi cholinga choti ophunzira m’sukulu zosiyanasiyana aziphuzitsidwa mokwanira momwe angamasamalire zachilengedwe pofuna kuthana ndikusintha kwa nyengo m’dziko muno.
Nduna yoona zachilengedwe ndi kusitha kwa nyengo mai Halima Daudi amalakhula izi mu nzinda wa Lilongwe pamwambo wotsekulira msokhano wa wa bungwe lolimbikitsa za maphunziro a zachilengedwe kumwera kwa Africa, la Environmental Education Association of southern Africa. Ndunayi yatsindika kuti dziko lino likukumana ndi mavuto ambiri pa nkhani yokhudza zachilengedwe