Kafukufuku wina yemwe akuluakulu ena achita m’dziko la America akuti akuwonetsa kuti akhristu ambiri a mpingo wa Katolika akukonda mtsogoleri wa mpingowu pa dziko lonse Papa Francis.
Ngakhale kuti Papa Francis sanakhale pa udindowu kwa nthawi yaitali, 79 mwa akhristu 100 aliwonse akuti akumukonda kwambiri m’dzikolo. Malinga ndi malipoti a Catholic Culture akhristu 4 mwa 100 aliwonse ndi omwe sakukonda papa Francis pomwe ena otsala sakuonetsa mbali yomwe akukonda pa utsogoleri wa Papa Francis. 83 mwa akhristu 100 aliwonse a mdzikolo akuti ndi omwe ankakonda Papa Benedict wa 16 opuma. Mzaka za m’mbuyomu 90 mwa akhristu 100 aliwonse a mpingo wa Katolika mdziko la America akuti ankakonda kwambiri Papa Yohane Paulo wachiwiri zomwe sizinachitikeko.