Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Boma lipitiriza kulanda maukonde osavomerezeka kuphera nsomba ku Nyanja ya Malawi

$
0
0

Boma lati lipitiriza kulimbikitsa kampeni yoteteza nsomba polanda maukonde osavomerezeka kuchokera kwa asodzi pofuna kuthana ndi mchitidwe wochita usodzi mosatsatira malamulo omwe ukuchititsa kuti chiwerengero cha nsomba chitsike kwambiri m’nyanja ya Malawi.

Wachiwiri kwa mkulu mudipatimenti yowona zachitukuko cha nsomba mu unduna wa malimidwe Dr Steve Donda amalankhula izi ku Monkeybay m’boma la Mangochi potsekera maphunziro a anthu omwe amagwira ntchito yoteteza nsomba m’nyanja za mdziko muno. Maphunzirowo  anabweretsa pamodzi anthu omwe amagwira ntchitoyi m’maboma onse omwe ali m’mbali mwa Nyanja za Malawi, Chirwa komanso mtsinje wa Shire ndipo anakonzedwa ndi boma la Malawi ndi thandizo landalama kuchokera ku bungwe la European Union (EU) kudzera ku bungwe la Smart Fish.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>