Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wauza akuluakulu a mpingowu owona za utumiki kuti kusamalira anthu ndi njira imodzi yosamaliranso chilengedwe.
Malinga ndi uthenga omwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu watumiza ku msonkhano wa akuluakuluwa omwe umachitikira ku likulu la mpingowu ku Vatican Papa wati popereka chisamaliro kwa anthu achichepere ngakhalenso ofowoketsetsa ndi koyeneranso kusamalira malo amene iwo akukhala.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati pa kusamalira chilengedwechi anthu okhudzidwawa azikhala umoyo wabwino komanso mmalo osamalilika.