Apolisi m’boma la Dowa akusunga m’chitokosi bambo wina wa zaka 34 zakubadwa kwamba komuganizira kuti wagwilira mwana wa zaka 12m’bomalo.
Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Richard Kaponda bambo-yu Amosi Mbewe anatenga mwana amene wamugwilila-yu kwa makolo ake m’mudzi mwa Kalewa m’dera la mfumu yayikulu Chiwere m’bomalo ndi cholinga choti azikamusamalira koma akuti wakhala akumuopseza ndi kumachita naye zadama kuyambira mwezi wa June chaka chino.
Nkhani-yi inaululika pa 4mwezi uno pomwe mkulu-yi anachitanso zadama ndi mwanayi ndi kumupatsa K100 kuti asaulure koma kamba ka ululu umene amaumva potsatira zadama zomwe bambo-yo anamuchita mwanayo anayamba kulira ndipo anthu oyandikana ndi nyumbayo atamufunsa mwanayo sanaope koma kuulura zoti bambo-yo anamugwililira.
Malingana ndi malipoti zotsatira zakuchipatala cha Salima komwe m’tsikanayu anapita naye zinasonyezanso kuti anamugwililadi.
A Amosi Mbewe akaonekera ku bwalo lamilandu posachedwa ndi kukayankha mulandu wogwilira womwe ndi wotsutsana ndi gawo 138 la malamulo oweluzira milandu m’dziko muno.