Anthu m’boma la Mwanza awapempha kuti adzizidalira pantchito ndi cholinga chotukula miyoyo yawo komanso kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino.
Bwanankubwa wa Bomalo a Gift Rapozo ndiomwe analakhula izi pa mwambo wogawa mbuzi kwa alimi omwe bungwe la Malawi Interfaith Aids Association (MIA) linapereka m’bomalo.
“Anthu olimbikira okha ndi amene angathe kupindula patchito zachitukuko zomwe zingathandize kupititsa patsogolo chuma cha dziko lino”. atero a Rapozo.