Mamuna ndi mkazi wake ati afa chiphaliwali chitawaomba mmudzi mwa Chilinda kwa mfumu yaikulu Makanjira m’boma la Mangochi.
Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergent Amina Daudi wauza Radio Maria Malawi kuti mamunayo Yusuf Mbalako wa zaka 66 zakubadwa ndi mkazi wake Annie Akibu wa zaka 56 zakubadwa anapita ku dimba lawo komwe mvula inawapezelera ndipo anaganiza zobwelera kunyumba kwao.
Sergent Daudi ati anthu awiriwa ali mu njira, chivomerezi chinawaomba ndipo atathamangira nawo ku chipatala chaching’ono cha Makanjira, atawapima anapeza kuti amwalira kaamba ka chivomerezicho.
Anthu awiriwa amkachokera m’mudzi mwa Chilinda kwa mfumu yaikulu Makanjira m’boma lomwelo la Mangochi.