Anthu okhala m’boma la Mangochi ati akukumana ndi mavuto kuti agule fetereza otsika mtengo wa makoponi chaka chino.
Izi zadziwika pamene Mtolankhani wathu anafika ku malo ogulitsira feterezayu komwe anapeza anthuwa ali m’mizere itali itali kuti agule feterezayu pa malonso omwe ndi amodzi okha a m’bomali a kampani ya Agora.
M’modzi mwa anthu omwe anali pa mzere kuti agule feterezayu a John Musianafotokozera mtolankhani wathuyu kuti anthuwa akukakamizidwa kugula feterezayu pa mtengo wokwelerapo wa 7, 500 kwacha pa thumba lililonse m’malo mwa mtengo wovomerezeka wa 7,000 kwacha.
“Anthu ambiri akumabwelera osagula fetereza chifukwa akubwera ochepa. Feterezanso akugulitsa 7, 500 kwacha mmalo mwa 7,000 kwacha ndiye kuti matumba awiri ndi 15, 000 kwacha koma ku Koche akugullitsa 8,000 kwacha thumba lililonse,” anatero a Musi.
Kenaka Mtolankhani wathuyu anafuna kulankhula ndi nduna ya za malimidwe mdziko muno Dr. George Chaponda koma zinakanika ndipo mneneri wa undunawu a Hamiton Chimala samayankha lamya yawo.