Quantcast
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ana Awiri Akokoloka ndi Madzi a Mvula

Ana awiri akokoloka ndi madzi a mvula mu mtsinje wa Thang’ande m’boma la Neno.

Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Raphael Kaliati wati anawa ndi Aufi Chiwembukomanso Benina Matemba onse a zaka zitatu ndipo patsikuli anatengana ndi azibale awo awiri a zaka 6 Ellisa komanso Ellina ndi kuwatsatira agogo awo ku munda ndipo akubwelera mvula inayamba kugwa kwambiri ndipo anapeza mtsinjewu utadzadza ndi madzi.

Atsikana okulirapowo anakwanitsa kuwoloka koma ana awiriwa anakanika ndipo anakanena kwa akuluakulu omwe anayamba kufufuza anawa koma sanawapeze.

Pa 19 ndi pomwe thupi la Aufi linapezeka mbali mwa mtsinje wa Makali koma thupi la Benina silinapezekebe mpakana pano.

Pakadali pano apolisi m’bomali apempha makolo kuti asamalore ana awo kuwoloka mitsinje okha kapena kusamba kuti apewe ngozi za mtunduwu mu nyengo ino ya mvula.

Iwo achenjezanso anthu onse omwa mowa kuti asamawoloke mitsinje ataledzera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>