Ansembe a mpingo wa katolika mu dayosizi ya Mangochi awapempha kuti alimbikitse umodzi pakati pawo ndi cholinga choti athe kutumikira bwino akhristu awo.
Wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la ansembe mu dayosiziyi la Association of Diocesan Clergy of Mangochi (ADCOM) bambo Lazarus Girevulo ndi omwe anena izi potsekulira msonkhano wa pa chaka wa ansembe a mudayosiziyi womwe ukuchitikira ku nyumba ya episkopi wa dayosiziyi.
Iwo ati pambuyo pa msonkhanowu ansembewa akhala ndi m’bindikiro wosinkhasinkha za moyo wawo wa uzimu.
Bambo Girevulo ati zimenezi zithandizo ansembewa kuti akatumikire bwino akhristu m’maparishi awo osiyanasiyana m’chaka chikubwerachi.
“Timakhala ndi m’bindikiro chaka cndi chaka kuti tiwunikirane momwe takhalira mchakachi komanso kukonza za momwe tikuyenera kukhalira mchaka chikubwerachi. Zimenezi zimathandiza ife ansembe kulingalira moyo wathu wa thupi komanso wa uzimu ndipo zimatithandiza kuti tikathe kutumikira akhristu athu moyenera mmaparishi mwathu mosiyanasiyana,” anatero bambo Girevulo.
Iwo anapempha ansembewa kuti asatayilire koma azikumbukira malonjezo awo a unsembe ponena kuti anavomera okha chiyitanidwechi.
“Ansembe asaluze focus, azichita zinthu modzindikira kuti ali ndi responsibility yaikulu. Ayike chidwi chawo pa utumiki wawo ngati ansembe chifukwa atayitanidwa anavomera okha. Asatengeke ndi zinthu za makono zomwe zingasokoneze utumiki wawo,” anatero bambo Girevulo.