Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Ambuye Tambala Apempha a Misala Asataye Mtima

$
0
0

Episkopi wa dayosizi ya Zomba ya mpingo wakatolika Ambuye George Tambala wapempha anthu amene amadwala matenda a misala kuti asamakhale otaya mtima koma azikhala okhulupilira komanso okonda kupemphera.

Ambuye Tambala amalankhula izi pomwe anakayendera anthu odwala matendawa ku chipatala cha anthuwa mu mzinda wa Zomba.

Iwo ati anthu omwe ali ndi matendawa akuyenera kumapemphera ndi chikhulupiliro komanso akuyenera kuzindikira kuti mpingo uli nawo limodzi.

Pamenepa Ambuye Tambala apempha anthu onse omwe ali ndi achibale omwe amadwala matenda a misala kuti aziwapatsa chisamaliro choyenera.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko