Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Wapempha Anthu a Mdziko la DRC Akhale Odezetsa Mtendere

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu a mdziko la Democratic Republic of Congo (DRC) kuti akhale okhululuka komanso odzetsa mtendere.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, Papa amalankhula izi lachitatu ku likulu la mpingowu pa mkumano omwe amakhala nawo ndi anthu osiyanasiyana omwe amakayendera malowa komanso pomwe kusamvana kwa pakati pa zipani za ndale kukupitilira mdziko la DRC.

Papa wapempha atsogoleri a ndale a dzikolo kuti achite zinthu zoyenera kuti athetse zovuta zimene anthu a mdzikolo akukumana nazo.

Iye walonjeza anthu a mdzikoli kuti apitiriza kuwathandiza ndi kuwaonetsera chikondi.

Malipoti a bungwe lowona za mgwirizano wa maiko la United Nations UN ati anthu oposera makumi awiri afa potsatira kusamvana komwe kunalipo pakati pa anthu owukira boma ndi magulu odzetsa chitetezo mdzikolo kaamba koti mtsogoleri wa dzikolo a Joseph Kabila sanatule pansi udindo wao pomwe amayenera kutero lolemba lapitali, ndipo m’malo mwake ati akhala akulamulira dzikolo mpaka chaka cha 2018pomwe kudzakhale chisankho cha Pulezidenti cha dzikolo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>