Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

WHO Ikhazikitsa Katemera wa Ebola Pofika 2018

$
0
0

Bungwe lowona za umoyo la World Health Organisation (WHO) lati pofika chaka cha 2018 likhala litakhazikitsa katemera woteteza anthu ku matenda a Ebola.

Malipoti a wailesi ya BBC ati padakali pano bungweli lapereka  nkhani ya katemerayu kwa magulu oyenera ndi cholinga choti avomerezedwe.

Malinga ndi malipoti ntchito yoyesera katemerayu yomwe inachitika mdziko Guinea lomwe linagwidwa kwambiri ndi matendawa, yasonyeza kuti katemerayu ndi othandiza kaamba koti anthu 6 sauzande omwe analandira katemerayu sanadwale matendawa patatha masiku khumi ndipo ena omwe sanalandire nawo katemerayu omwenso anali mu gulu la anthuwa, makumi awiri ndi atatu 23 anadwala matendawa.

Padakali pano sizikudziwika ngati katemerayu angagwire bwino ntchito kwa ana kaamba koti sanayesedwe.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875