Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wauza atsogoleri a mpingo kuti akuyenera kuzindikira kuti chikondwelero cha khrisimasi ndi nthawi yokondwelera kudzichepetsa kwa chikondi cha Mulungu.
Papa amalankhula izi lachinai pa msonkhano omwe anali nawo ndi atsogoleri a mpingo a kulikulu la mpingowu.
Pa msonkhanowu Papa anauza atsogoleriwa kuti akuyenera kumanga umodzi ndi cholinga choti mpingo ukule mu ntchito zake.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati Papa wapemphanso atsogoleriwa kuti akuyenera kusintha kaganizidwe kawo kaamba koti kupanda kutero mpingo supita patsogolo ndi ntchito zake.
Msonkhanowu unachitika pa mutu wakuti “Kukhazikitsa njira zogwilira ntchito ndi zomwe zikuyenera kubwera pambuyo potsatira njira zogwilira ntchitozo.”