Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Papa Franscisco Apempha Achinyamata kuti Asabwelere Mmbuyo ndi Chikhulupiliro Chawo.

$
0
0

Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wauza achinyamata kuti asalole wina aliyense awasochotsere mu chikhulupiliro chao mwa Mulungu.

Malinga ndi uthenga omwe mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu watumiza kwa achinyamata a mdera la Taize mdziko la France omwe akakhala nawo pa msonkhano wa achinyamata a mmaiko a ku ulaya mu mzinda wa Riga mdziko la Latvia, Iye wayamikira achinyamata onse omwe akakhala nawo pa msonkhanowu ndipo kuti kubwera kwao kwasonyeza kuti sangalole kuti wina aliyense awapangire tsogolo lawo.

Papa wapempha achinyamatawa kuti akhale ozama mu chikhulupiliro chao mwa Yesu Khristu kamba koti iye sakhumudwitsa.

Iye wati ngakhale ena amabwelera mmbuyo kamba ka zamtopola ngakhalenso mavuto omwe anthu ena akukumana nawo, iye wapempha achinyamatawa kuti atengepo gawo pothetsa zinthu za mtunduwu.

Pamenepa Papa wati akukhulupilira kuti msonkhanowu, uthandiza achinyamatawa kuti asamakhale mwa mantha komanso akule mu chikhululupiliro ndi chiyembekezo mwa Yesu Khristu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>