Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wati ndi okhudzidwa ndi zamtopola zomwe zachitika pa ndende ina zomwe zaphetsa anthu oposera makumi asanu 50 mdziko la Brazil.
Papa amalankhula izi lachitatu pa mkumano omwe amakhala nawo ndi anthu okayendera likulu la mpingo wakatolika ku Vatican ndipo anayikiza mmapemphero anthu onse omwe amwalirawa, mabanja awo, anthu omwe akusungidwa pa ndendeyo ngakhalenso ogwirapo ntchito.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican Papa wati kundende ndi kumalo kumene anthu amaphunzira komanso kusinthikira makhalidwe.
Polankhulapo nduna ya zachilungamo mdziko la Brazil yati dzikolo likuyenera lichitepo kanthu pa nkhani ya chisamaliro cha ndende zawo.