Ndege ina ya mdziko la Egypt yomwe imachokera mu mzinda wa Paris kupita mu mzinda wa Cairo ati yasowa mu mlengalenga itanyamula anthu okwana 66.
Malinga ndi malipoti ndegeyo ati yasowa kuzambwe kwa nyanja ya Mediterranean itangolowa kumene mu mlengalenga kwa dziko la Egypt.
Malipoti a wailesi ya BBC ati kampani ya ndegeyo inalandira chenjezo la vuto lomwe ndegeyo imakumana nalo isanasowe.
Padakali pano asilikali a dzikolo mogwirizana ndi a mdziko la Greece akufufuza ndegeyo ndipo dziko la France lalonjeza kuti litumiza ma bwato ndi ndege zoti zithandizire pa kafukufukuyi.