Ophunzira omwe ali ndi vuto lakusawona pa sukulu ina m'boma la Mulanje apempha bungwe la Malawi Electoral Commission MEC kuti liwapititsire zipangizo za Brail kuti iwo adzathenso ku vota bwino pa zisankho za chaka cha mawa.
Ophunzirawo amalankhula izi pa msonkhano omwe ofesi ya za chisankho mbomalo komanso bungwe la NICE linachititsa pofuna kuthandiza ophunzira omwe ali ndi vuto lakusawona kuti atengepo gawo polembetsa mu kaundula wa zisankho. Poyankhulapo mmodzi mwa ophunzira omwe ali ndi vuto lakusawona pa sukuluyo anapempha bungwe la MEC kuti liwapitilitse zipangizo zomwe zingawathandize kuti adzathe kudzavota ngati mmene zinalili pa zisankho za mmbuyomu. Poyankhulapo mmodzi wa anthu ogwira ntchito ku khonsolo ya boma la Mulanje a Thom Nthali anati ayesetsa kufotokozera bungwe la MEC kuti likwanilitse udindo wawo pothandiza kuti anthu omwe ali ndi vuto lakusawona adzathe kuponya bwino voti. Mkulu a bungwe la NICE mbomalo a Twambilire Mwabungulu anati ndi udindo wa aliyense kusankha atsogoleri abwino omwe angathandize pa chitukuko cha dziko lino