Sub T/A Nkangula ya m'boma la Zomba yati kusankhidwa kwa makhansala pa zisankho za chaka cha mawa kuthandiza kuchepetsa ntchito yomwe mafumu akhala akugwira zomwe zithandize pa chitukuko cha dziko lino.
Mfumuyi yanena izi polankhula ndi mtolankhani wa zachisankho mbomalo. Sub T/A Nkangula yati mafumu akhala akugwira ntchito zambiri zomwe khansala amayenera kumagwira ndipo kusankhidwa kwa makhansala kuthandiza kuti ntchito zina zachitukuko zidziyenda bwino. Mfumuyi yathokozanso aphungu ena omwe akhala akugwira bwino ntchito zachitukuko ndi mafumu ena mmadera osiyanasiyana.