Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Akatolika Mdziko La India Apempha Boma Litenge Gawo Mpaka Bambo Tom Apezeke

$
0
0

Akhristu a mpingo wakatolika mdziko la India apempha boma la dzikolo kuti likambirane ndi maiko a mchigawo chapakati chakuzambwe ndi cholinga choti atulutse bambo Tomomwe anagwidwa mdziko la Yemen ndi zigawenga za chisilamu za Islamic State mmwezi wa March chaka chatha.

Malinga ndi kalata yomwe bungwe la akhristu eni ake mdzikoli lalembera nduna yaikulu ya dzikolo a Narendra Modi yomwe yasainidwa ndi pulezidenti wa bungweli a Lancy Da Cunha akhristu mdzikolo apempha boma kuti lilowelerepo pa nkhaniyi ndi cholinga choti Bambo Tom atulutsidwe komanso abwerere kwao ali bwino.

Bambowa anagwidwa pomwe gulu la za uchifwambali linakachita chiwembu pa malo ena omwe kumakhala anthu odwala ndi okalamba komwe anapha asisteri anayi a chipani cha Tereza komanso anthu khumi ndi awiri omwe anali ku malowo pa nthawiyo.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>