Bwalo la magistrate ku Namwera mboma la Mangochi lalamula mzika ya zaka 37 ya mdziko la Mozambique, Jairosi Duwa kukakhala kundende chifukwa chopezeka ikugulitsa mafupa a munthu kwa munthu wina wabizinesi wa kwa mfumu yayikulu Bwananyambi mbomali.
Malinga ndi mneneri wa apolisi mboma la Mangochi Inspector Rodrick Maida, izi zinachitika pa 20 february. Pa tsikulo Duwa yemwe kwawo ndi mboma la Mandimba ku Mozambique anakumana ndi Amos Jasten ndi kumutsatsa mafupi a munthu pa mtengo wa Mk900,000.
Malinga ndi Inspector Maida, wabizinesiyu anawonetsa chidwi chogula mafupawo ndipo anagwirizana kuti akakumane ku Namwera komwe akapereke ndalama koma atatero anadziwitsa apolisi za nkhaniyi. Atafika ku Namwera bamboyu anafikira mmanja mwa apolisi.
‘’Apolisi anamanga bamboyu chifukwa chopezeka ndi mafupa a munthu ndipo bwalo la milandu ku Namwera linagamula kuti akagwira ukaidi kwa miyezi itatu komanso kupereka chindapusa cha Mk3000 kulepherapo zonsezi kuti akakhale kundende kwa miyezi isanu ndi itatu’’. Anatero a Maida.
Malinga ndi Inspector Maida zomwe bamboyu anachitazi sizichitikachitika.