Mtsogoleri wa dziko la Phillipines Rodrigo Duterte wakanitsitsa kuvomeleza maukwati a amuna kapena akazi okhaokha.
Malipoti a wailesi ya BBC mtsogoleriyu wakanitsitsa kuti sangavomereze mchitidwewu ngakhale kuti azibale ake ambiri amachita mchitidwewu.
Izi ati zadzetsa mpungwepungwe pomwe ena mwa atsogoleri a ndale mdzikolo akuti mtsogoleriyu amayenera kuvomereza mchitidwewu mdzikomo.
Pakatipa mtsogoleriyu ati wakhala akulimbana kwambiri ndi anthu ochita malonda a mankhwala ozunguza bongo mdzikolo.
Iye wadzudzula maiko a chigawo cha kumadzulo kaamba komakakamiza dziko la Phillipines kuti lizichita zinthu zina zomwe silikufuna zomwe ndi zosemphana ndi zikhululupiliro zawo.