Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wapempha ansembe kuti ayike sakramenti la kulapa patsogolo kuti alimbikitse umoyo wa uzimu mma parishi mwawo.
Papa Francisko amalankhula izi ku likulu la mpingowu ku Vatican kwa anthu omwe anasonkhana pa maphunziro a pa chaka okhudza sakramenti la kulapa.
Iye wapempha ansembe kuti azipereka sakramentili pa nthawi iliyonse yomwe munthu wawapempha kuti akufuna kulapa osati kungokhazikitsa masiku ochepa okha pa mulungu operekera sakramentili.
Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu wati ansembe kuti athe kupereka bwino sakramentili akuyenera kukhala okonda kupemphera, pakhale ubale wabwino pakati pa iwo ndi mzimu woyera komanso akhale abusa abwino.