Nyumba zowulutsa mawu za m’madera a kumidzi (Community Radio) azipempha kuti zizipereke pa ntchito yofalitsa mauthenga a njira zopewera matenda a kolera omwe amafala kwambiri mu nyengo ya mvula.
Mmodzi mwa akuluakulu mu unduna wa zaumoyo mdziko muno a Elton Chidothi Banda anena izi m’boma la Kasungu potsekera maphunziro a tsiku limodzi othandiza atolankhani za udindo wawo pa ntchito zolimbana ndi kufala kwa matendawa mdziko muno.
A Banda ati ngakhale kuti dziko lino likuchita bwino polimbana ndi matenda a kolera, ma wailesi akuyeneranso kupitiriza kumwaza mauthenga kuti mbiri ya kupezeka kwa matendawa ikhale ya makedzana.