Nduna ya zophunzitsa anthu mai Patricia Kaliati wapepha mabanja kuti athandizire Radio Maria Malawi kufalitsa nthenga wa chipulumutso mu njira zosiyanasiyana.
Mai Kaliati amalankhula izi ku parish ya Balaka pomwe Radio Maria Malawi imachita mwambo wotsekulira Mariatona komanso pomwe mpingo wa katolika umachita chaka cha nthenga wa mnjelo kwa Amayi Maria.
Iwo ati banja likakhala la makhalidwe osayenera, nkhani ya mayitanidwe kwa anthu ena a m’banjamo imaponderezedwa.
Mayi Kaliati ati pamene Radio Maria Malawi ikugwira ntchito yake yofalitsa uthenga wabwino, ana nawonso akuyenera kulandira uthengawu ndi kuwugwiritsa ntchito moyenera.
Polankhulapo mkulu woyendetsa mapologalamu ku Radio Maria Malawi bambo Joseph Kimu athokoza anthu onse omwe atenga mbali patsikuli ndipo ati ali ndi chikhulupiliro kuti mariatona-yu ayenda bwino.