Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Dayosizi ya Mangochi Ikufuna Akhristu Apindule ndi Nyumba Zake Zowulutsira Mawu

$
0
0

Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Mangochi yati ikufuna igwiritse bwino ntchito nyumba zowulutsira mawu zomwe ili nazo pofalitsa nthenga wa Mulungu.

Episkopi wa dayosiziyi Ambuye Montfort Stima ndi omwe anena izi pa mkumano wa nthumwi za nyumba zowulutsira mawu za mu dayosiziyi komanso akuluakulu ena a dayosiziyi.

Iwo ati akufuna kuti akhristu a mu dayosiziyi akhale akupindula ndi nyumba zowulutsira mawu zomwe ali nazo.

Polankhulapo mkulu wa kuofesi yoona zofalitsa nkhani mu dayosiziyi bambo Emmanuel Malipa ati dayosiziyi ndi yokonzeka kupereka mauthenga oyenera kuti akhristu azimva zinthu zolondola zokhazokha.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>